Patson Team worker's
19/03/2026
Apolisi mu mzinda wa Mzuzu amanga Lovemore Manase Hara wa zaka 19, pomuganizira mulandu wothyola nyumba ndi kuba katundu.
Wachiwiri kwa m'neneri wa polisi ya Mzuzu, Sergeant Edson Chipeni watsimikiza za kumangidwa kwa Hara ponena kuti apolisi amanga nkuluyu, kutsatira dandauro lomwe analandira pa 18 Mwezi uno kuchokera kwa a Tiwonge Mtonga kuti munthu wina wathyola ndi kuba katundu m'nyumba yawo.
Malingana ndi Chipeni apolisi atachita kafukufuku pa nkhaniyi akwanitsa kumanga oganizilidwayu ndi kulanda katundu wobedwayu ndipo nzake wa oganizilidwayu wathawa.
Wina mwa katundu obedwayi ndi kanema wa Samsung 55 inches, zoimbira ziwiri, lamya zamakono ziwiri, zipangizo zosungira nyimbo ziwiri (flash discs), chofunda, ndalama yokwana K15 000 komanso thumba la chomanga lolemera makilogalamu 10 ndipo zonse ndi za ndalama zokwana K3.5 million.
Chipeni wati oganizilidwayu wauza apolisi kuti anathyolanso nyumba ndi kuba katundu wa a Anold Soko ochokera kwa Kampingo Sibande m'boma la Mzimba ndipo padakali pano katundu obedwayu wapelekedwa ka eni pamene oganizilidwayu akuyembekeza kukayankha mulandu wothyola nyumba ndi kuba katundu.
Wolemba;Collins Mulele-Mzuzu
Danabai project
we are moving forward
Danabai project we are busy down frool
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Telephone
Website
Address
Zone 7 Thembalethu
George