The Masilo
17/10/2025
Aliyese azinena zomwe akuona kwa nyamata mukumuona apayi wakuzombaa.
zikuchitika ndithu
16/10/2025
Malipoti osatsimikizika kuchokera ku Chipani cha DPP ati akuluakulu a Chipanichi akhumudwa ndi ganizo la mtsogoleri wa Chipanichi a Peter Mutharika losankha a Sameer Suleiman ngati yemwe apikisane pa mpando wa sipikala wa Nyumba ya Malamulo
Izi zikudza pomwe akuti ambiri anasankha Dr Ben Phiri ngati womwe akuyenera kupitkisana pa mpandowu
A Phiri akuti anali atayamba kale kukonzekera pa mpandowu
16/10/2025
Mrs Namadingo
16/10/2025
Rise for Phoka is a Community Based Foundation which is in Livingstonia,Rumphi. The organisation focuses on community activities,education and elderly companionship among others, I f you have time visit them,learn and know more about them.
Today on 16 October, Rise for Phoka is cerebrating World Food Day with the theme
visit their website at www.riseforphoka.org
email: [email protected]
13/10/2025
Ndalama zokwana K25 million ndi zomwe zagwiritsidwa ntchito kujambula kanema wotchedwa Chitomero yemwe muli atengambali odziwika bwino monga Ginte, Phwedo komanso Mphatso Machira.
Ndalamayi anaipereka ndi mkulu wina wa mdziko la America kuti zonse zokhudza kanemayu yemwe muli atengambali oposa 40 ziyende bwino.
Phwedo yemwe analemba nkhani ya kanemayu wati kanemayu alunjika kwambiri pa nkhani ya chikhalidwe cha dziko lino ndipo yajambulidwa malo akumudzi kokha.
Phwedo watinso mkanemayu Ginte achita khalidwe lake lopezeka malo a akabanga (Mowa) pomwe iyeyu ndi Mphatso Machira asintha makhalidwe awo.
Woyimba Malita ndi yemwe wakonza kanemayu ndipo naye watenganso mbali mkanemayu.
Kanema wa Chitomero atulutsidwa mwezi wa mawa koma kachidutsa kake katuluka masabata awiri akubwerawa.
Neria Chikhosi, Yvonne Scott, Pamela mwenisungo, Everisto payesa ndi enanso mwa atengambali omwe ali mkanemayu.
13/10/2025
Ati Mudzi omwe ajambulira kanema uyu adachita kumanga okha.
Iyi ndi Movie ya ‘CHITOMERO’ imene muli oyimba zachikhalidwe, Malita ndi akatswiri opanga mafilimu odziwika bwino m’Malawi monga Phwedo, Ginte komanso Mphatso Machira.
Chitomero ndi mwambo umene wakhala ukudziwika bwino kwambiri mudzaka za mbuyo kotero Chitomero ndi movie yomwe ikufotokoza za Chikhalidwe cha chiMalawi.
Filimu imeneyi ikhala ikutuluka mu November 🎥
12/10/2025
President APM ndi Chipani cha DPP chasankha Hon Suleman ngati candidate wa Speaker ya nyumba yamalamulo.
12/10/2025
A Malawi ambiri amusowa Timothy Mtambo, akungofuna atatulukira
Mawu amodzi kwa Comrade
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Website
Address
Zomba