Latest from Edmond Bitoni
Pa chipatala chathu cha Thyolo pali vuto lalikulu la ukhondo.
Izi ndi kamba kakuonongeka kwa ma flashing toilets, vuto la madzi a water board.
Mwachitsanzo, ward imodzi yomwe mumakhala odwala opitilira 30, imagwiritsa ntchito toilet Imodzi yomwenso ndi yoonongeka.
Munthu akagwiritsa ntchito toilet yi akuyenera atunge madzi akathire kuti zoipazo zipite pansi.
Zaonetsa kuti vutoli ndi la pa ka nthawi.
Koma nanga adindo akutiponji?
BWENZI LA KU MTIMA
Ndalipeza langa bwenzi la Ku mtima
Bwenzi londigudulira chikondi mosasinila
Bwenzi lopanda banga
Bwenzi losatopa, inde lopanda nsanje
Bwenzi la Ku mtima
Mwa iye chinyengo mulibe
Bwenzi lokoma mtima,
Nlofafaniza tchimo la dziko la pansi
Ndikupereka wosatha moyo
Bwenzi la ku mtima
Ndi mchilikizo weni weni wa moyo wanga
Bwenzi losandi inga
Pa msautso, pa mtendere, tikhala nganga
Anga chitseko mferemu
Bwenzi losakhumudwisa
Pakuomba namondwe anditeteza
Ndikatelereka andigwira dzanja
Bwenzi la ku mtima
Lotaya wake moyo,
Pokhetsa mwazi pa calvary paja
Chifukwa cha wanga moyowu
Paja pa Gologota,
Pofunitsitsa kuti ndikhale mfupi naye
Dziko pokana kuunika, potsata mdima
Inde lindikonzera malo m'mwamba
Bwenzi la ku mtima
Langa thandizo lopezekelatu
N'kamva njala, andininkha mkate
Mkate wa wamoyo
Ndikamva ludzu, andikonkha madzi kukhosi
Madzi ondininkha moyo
Aja adamulonjeza namwali wa ku Samaria
Pa chitsime pajaaa
Bwenzi la ku mtima
Mpulumutsi wolonjezedwa, mau ofuula nchipululu
Kalonga wa mtendere,
Mfumu ya mafumu
Mamuna wantanda wa moyo
Woyesedwa katatu ndi mdielekezi,
Wogonjetsa imfa masiku atatu
Mchilisi wanga Ndikamva litsipa
Andipyoletsa mu nthunzi wa imfa
Inde andimenyera nkhondo,
Nalesa namondwe powomba
Bwenzi la ku mtima
Ndie mukandipenya kudekhaku,
Chimwemwe chodzadza sayachi,
Makolasi pakamwapa,
Bayibulo kudzanjaku,
Ndakatuloyinso iyi,
Dziwani Ndalipeza langa.
BWENZI LA KU MTIMA
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Website
Address
Thyolo