God's Embassy Rabbi Ministries
Faith without work is dead faith
12/05/2026
Abale
Tiyeni tiyimebe mu chikhulupiliro posatengera nyengo yomwe tidutsamo m'masiku ano wotsiliza. Tili mu nthawi yomwe malemba adachenjezeratu kuti mavuto adzakhala akuchulukirabe. Ndipo ambili adzataya chikhulupiliro chifukwa Cha nyengo zomwe akudutsamo koma ife tiyeni tiyimebe mu chikhulupiliro ndi kusatekeseka pozindikira kuti mavuto onse ndi akanthawi kochepa ndipo tidutsa pokhala Mulungu ali nafe ndipo tilibe mantha.
Yesaya 43:1
1. Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israyeli, Usaope, cifukwa ndakuombola iwe, ndakuchula dzina lako, iwe uli wanga. 2. Pamene udulitsa pamadzi ndiri pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsya; ngakhale lawi silidzakutentha.
Fellow believers,
Let us live out our faith by speaking positively about who we are in Christ, declaring blessings and not curses, with our words reflecting God's love and life, knowing the small yet powerful tongue can bring life and death.
Stay blessed🙏
04/05/2026
-highlights
Mu sabata imeneyi tiyeni tiyende ndi Yesu amene atitsimikizirw ife za Moyo wosatha kwa muyaya.
Performance by: Muntchi choir
10/04/2026
📖📖📖📖📖📖📖
Ezekieli 15:5 "Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?"
Uwu ndi mtengo wampesa, sunapindule unakali wanthete ndi osapsa, nanga kuli kotani moto utautentha, ndikuupsereza?
Muli bwino choncho, muli wangwiro m'malingaliro, muli ndimphamvu choncho, mukukwanisa kuzichitira nokha zinthu, opani mawa, konzekerani mawa.
Fesani mbewu yabwino m'moyo wanu, khalani pamtendere ndi anthu ndi banja lanu, chitani chokoma, funirani ena zabwino, zichepeseni m'moyo uno, ndipo opani Mulungu.
Kodi mukudziwa kuti m'moyowu pali nthawi ngati iyi:
Yohane 21:18 "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita."
Nthawi imeneyi imafika, zomwe sunadzifune zimatha kufika, nyengo imene sunayiyembekeze imatha kufika, moyowu pena mphamvu zimatha, kudziwa kumatha, kuchenjera kumasanduka kupusa, kudzikuza kumachepa.
Ngati mukulephera kukhala bwino munthawi yanu yanthete, moto ukadzakupserezani muzakhala pati!
Tsiku lililonse litengeni kukhala chisomo, ndikuyenda molondola kudziko lapansi. Yanjanani ndi Mulungu, khalani bwino ndi ena, opani mawa!!!
________________________
17/03/2026
2 MBIRI 24 : 2
"Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe."
Sibwino kuyika moyo wathu wa uzimu m'manja mwa munthu wina, tamvani za Yowasi amene anachita zolungama chifukwa Yehoyada anali moyo, atamwalira Yehoyada, Yowasi anabwelera m'mbuyo pamodzi ndi a Yuda onse.
2 Mbiri 24 : 18 "Iwo anasiya Nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anapembedza Asera ndi mafano. Chifukwa cha kulakwa kwawo, mkwiyo wa Yehova unabwera pa Yuda ndi Yerusalemu."
Mkofunikira kukhazikitsa ubale wathu wabwino ndi Mulungu, umene siudalira kapena kuyang'anira kupezeka kwa munthu kapena ayi, kapena zomwe ena akuchita. Funitsitsani kumudziwa Ambuye mwanokha, ndikukula mu chidziwitso chake tsiku ndi tsiku.
Akolose 1 : 10 "Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu."
_____________AMEN_______________
13/03/2026
Here we go, another opportunity to tap into a revelation that transforms life, GEM nothing but Truth all day!!!!
"Truth shall set us free, John 8:32"
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Website
Address
Lilongwe