Odalitsika
15/10/2025
Unduna woona za ubale wadziko lino ndi maiko ena watsimikiza kuti a Malawi 22 anali mu bus yomwe inachita ngozi ndikupha anthu oposela 40 Lamulungu usiku mu dera la Limpopo, ku South Africa.
Mu kalata yomwe yatuluka Lachiwiri usiku, undunawu wati wazindikira a Malawi 14 pomwe ena asanu ndi atatu akusowabe. Mwa omwe awazindikilawa, 8 akanali mu chipatala pomwe 6 awatulutsa.
Nyumba yofalitsa mawu ya BBC inalengeza lolemba kuti athu 42 afa pa ngozi ya bus m'mapiri ena pa msewu wa N1 mchigawo cha Limpopo. Bus-yo inali pa ulendo wobwera ku Malawi kudzera ku Zimbabwe, ndipo inanyamula nzika za Malawi ndi Zimbabwe.
Koma unduna-wu mu kalata yake wati anthu 43 ndiwo afa pangoziyo ndipo kuti bus-yo inanyamula anthu oposela 90. Undunawu sunapeze uthenga wa m'Malawi amene wamwalira pangoziyo koma wati akulu akulu a dziko la South Africa akuunikabe matupi kuti awazindikire.
Komabe, m'modzi mwa anthu ogwira ntchito ku ofesi ya kazembe ku South Africa-ko wauza Zodiak Online kuti ndizovuta kuzindikira anthu chifukwa ena analibe ziphaso zowazindikilitsa komanso ziphaso zoyendera.
(by John-Paul Kayuni-Lilongwe: 10/15/25)
HAPPY MOTHER'S DAY. osaiwala kutipanga follow Odalitsika mulungu amakhalanaye
BOMA NDILOMWELI PALIBE KUSINTHA
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Telephone
Website
Address
LILONGWE TO SALIMA
Lilongwe