Mjidi multimedia

Mjidi multimedia

Share

13/05/2022

Agwidwa ndi pangolin wamoyo.

Apolisi kunchinji amanga amuna awiri amandela masautso azaka 34 komaso a mavuto jophris azaka 33 atapezeka ndi pangolin wamoyo.
Mneneli wa apolisi kumchinji amaxwell jailosi ati iwo anamvetsedwa k*t awiriwo dzulo amachita malonda akanyamaka komwe anakaika musaka ndikukabisa muchikwama chobelekela kumbuyo.
Koma atafika pamalo ena ochitila malinda pa Bua apilisi omwe amayang'anila zachilengedwe komaso nyama zamkhalango anabwandila azibambo awiliwa ndikukawasunga muchitokosi cha apolisi.

02/05/2022

Kondwani Nankhumwa apatsa a chakwela masiku khumi ndi anayi.

Mtsogoleli wambali yotsutsa mnyumba yamalamulo, olemekezeka a kondwani nankhumwa lamulungu wapatsa mtsogoleli wadziko lino masiku khumi ndi anayi k*ti apeze njila zothana ndimavito azachumwa omwe ali mmdziko muno mdipo akhudza anthu ochuluka.
Poyankhula mu mawu omwe analankhula pamsonkhano wachitukuko omwe anachititsa kwa mgona mumzinda walilomgwe iwo ati nthawi yakwana k*ti achakwela atenge gawo kuyang'ana zinthu zikuluzikulu mdziko muno mmalo mowononga nthawi kumakayendela mbewu mmadela osiyanasiyana ndi zina.

20/04/2022

Apolisi agwila azibambo asanu ndi anayi omwe amawaganizila k*ti amachita zauchifwamba pa kachipeya moyandikana ndi msika wa lizulu mboma la ntcheu.
Anthuwa amatseka mseu wa M1 ndimiyala ndikumachita chifwamba anthu oyenda panjinga zamoto.
Mneneli wa apolisi mudziko muno, Harry Namwaza wati dzigawengadzi dzagwila mawona apitawo kucha kwalelo.
Anamwaza atiso zida zoopsa monga zikwanje zinapezeka ndi achifwambawa ndipo zalandidwa.

11/04/2022

Nduna yoona zamigodi a Albert Mbawala ati feteleza otsika mtenga anafika ku ntchewu koma mbeu zalephela kuchita bwino kamba ka ng'amba yomwe inachitika mbomali.
Ambawala atinso mabanja ambiri akufunika thandizo lachakudya mubomali.

Ambawala anatiso nkhani yakukwela mtengo kwakatundu anthu asazilowetse ndale chifukwa zinthu zavuta padziko lonse lapansi.
Iwo alankhula izi pamsonkhano wachitukuko umene mtsogoleli wadziko lino wachitsitsa muboma lantcheu mdela ya mfumu yaikulu makwangwala atamaliza kuendela mbeu mu dela ya mfumu yaikulu njolomole mubomalo

Want your business to be the top-listed Media Company in Lilongwe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Telephone

Website

Address


Kachere
Lilongwe