Islamic Issues II

Islamic Issues II

Share

09/06/2026

ZOMUYENEREZA MUNTHU KUTI SWALA YAKE IKHALE YOLANDILIDWA

Pempholo la MUNTHU mnsilamu Kuti lilandilidwe PAMASO pa Allah Pali zinthu zofunikila Kuti munthuyo azikwanilitse.
Zinthuzi zimatchedwa ( شروط الصلاة ) ndipo zilipo zisanu NDI zinayi 9.

Kusasamala mfundo 9 izi Swala singakhale YOLANDILIDWA.

Popeza mpovuta kutchula mfundo zonsezo tiyeni tingonena ya pa number 1.

الاسلام kukhala mnsilamu

Mfundo iyi ikuchokera pa aya iyi
فاقيم الصلاة ، ان الصلاة كانت علامامنين كتاب الموقوتا

👉 Imikana swala , ñdithudi swala inakhazikitsidwa Kwa anthu okhulupilila ( asilamu ) kuti ipempheledwe munthawi yoikika.

Kukhala mnsilamu NDI makiyi achilichonse Kwa Allah الله ndipo ngati munthu sikhala mnsilamu tchito iliyonse imapita pachabe.

Pamene munthu wapanga ,شاهاد ndiye watsekula khomo lakuti tchito zake zizilandilidwa kuphatikizilapo swala.

فجتنبو الشرك
Mnsilamu ophatikiza الله ndizinthu zinà swala yake imakhala yosalandilidwa.

Shirk imawononga tauhid
Tipewe zinthu zotitulutsa muchisilamu ,,, matalazimu, kuwombeza , kukhwama, kudalila nyanga.

Izi ndizinthu zimene ZIDAMPANGITSA munthu kuchoka chikonda Cha ,الله , kudalila Allah
Mkuyamba kudalila shayitwan.

U munafuq, ndizonse zotitalikitsa NDI الله ، cholinga tiziswali tilidi asilamu enieni kuti
Condition yoyamba ya swalayi ikhale yamoyo , ndikuti swala yathu izikhala YOLANDILIDWA pamaso pa الله

Pangani like page iyi ndikupanga share , kuti nkhani izi zifikile ambili , ndikuti nawo aphunzile nawo

,السلام عليكم

06/08/2025

NDI ANGATI AMENE TAKHALA TIKUNYOZA ANTHU OMWE AKWATILAPO MITALA?

Assalam alaycum

Machimo enawa tiziwapewa, mitàla kuchisilamu sitchimo ayi.

Choyenera kudziwa NDI chakuti Mulungu amadziwa ndipo ife sitimadziwa kanthu.

Kukwatila kuchisilamu NDI sunna osati FARADHWI.

Koma sunna yake ndiyofunikila kwambili yomwe kuisiya ukhoza kugwera kudzenje lauchimo.

Kukhala opanda mkazi sitchimo
Kukhala ndimkazi mmodzi ☝️ sitchimo
Kukhala nawo awili malile 4 sitchimo.

MNCHIFUKWA CHANI ANAIKA MALILE 4?

Sura 4v3 Allah mumnzeru zake Adaika malile akazi 4
Powona kuti ngati saika malile kudzakhala chisawawa chopanda discipline.

Tsono Allah akufuna chilungamo.
Ukwatila Kaya sukwatila bola ukhale wachilungamo
Osapanga zauhule.

Chilungamo chosamala akazi mofanana.

Tsono Allah pololeza mitala , osailetsa adawona zinthu izi

1. Mamuna amafuna mkazi nthawi zonse , mkazi safuna mamuna nthawi zonse.
2. Mkazi Ali ndi vuto la mnsambo ndi ubereki lomwe limapangitsa kusakhala NDI mamuna mwachikakamizo.
3. Munthawi yoletsedwa kukhala ndimamuna , ndinthawi yomwe thupi lamamuna limafuna popumila.
4. Akazi NDI ambili mnchilengedwe poyerekezera amuna.

Tsono inu mitala simumaikonda ayi
Chisakhale chiphinjo kwa iwo amene amaikonda.
Musawanyoze
Musawatukane
Musawaeruze.

Kutelo kuli ngati
Mwanyoza Allah ndi mtumiki wake
Omwe adaloleza
Mtumiki adapanga mitalayi

Tiyeni tipewe kulankhula zopanda umboni

بارك الله فيكم

05/05/2025

Mtumiki s.a.w adati , munthu yemwe abereke Mwana wamkazi mkumulera bwino
Mkumupilila mkaleledwe , mkumupezera mamuna wachisilamu

Adzakalowa ku janna

Atsikana chooonde musalore kukwatiwa ndi munthu yemwe sali mnsilamu.

Ndipo musapusitsike kuti akutsani ambiliwa NDI onama
Pempherani kuti muzapeze wa din wabwino.

Chonde amuna Inu pezani atsikana a chisilamuwa kuti Iwo apeze mwayi wabanja lachisilamu lodalilika

Allahumma Amin 🤲

Want your place of worship to be the top-listed Place Of Worship in Blantyre?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Telephone

Website

Address


Blantyre