Lonjezo Library

Lonjezo Library

Share

07/06/2026

SAD TRUTH
PART 4
WRITTEN BY LONJEZO SUMAN
FROM LONJEZO LIBRARY

PANGANI FOLLOW PAGE IMENEYI KUTI NKHANI ZANGA ZIZIKUPEZANI MOSAVUTA

M’mawa wotsatira, Daniel anadzuka ali ndi maganizo osokonekera. Kwa nthawi yoyamba m’miyezi yambiri, nyumba yawo inali ndi chakudya chokwanira. Grace ankaseka uku akuthandiza amayi awo kuphika tiyi, ndipo fungo la buledi wotenthedwa linadzaza m’nyumba yonse.

Koma Daniel sanape mtendere.
Nthawi iliyonse akaona ndalama zimene zinali m’thumba lake, mtima wake unkamenya mwachilendo.

Anadziwa kuti ndalama zimenezi sizinachokere ku ntchito yabwino.

“Daniel,” amayi ake anayankhula mofooka, “lero upite kusukulu.”

Daniel anayima kaye.
“Mama…”

“Usasiye maloto ako chifukwa cha mavuto.”
Daniel anayang’ana nkhope yawo yotopa. Ngakhale anali odwala kwambiri, ankayesabe kumulimbikitsa.

“Ndipita,” anayankha pang’onopang’ono.

Atamaliza kudya, anatenga chikwama chake chakale n’kuyamba ulendo wopita kusukulu. Koma tsiku limenelo zinthu zinkamveka zosiyana.
Anthu amene ankadutsa pafupi naye sankawoneka ngati kale.

M’maganizo mwake munkangobwera chithunzi cha Mr. Banda ndi ndalama zija.
Atafika kusukulu, Michael anathamangira kwa iye.

“Daniel! Dzulo sunabwere.”

“Ndinali busy.”

“Zikuyenda bwino bwino?”
Daniel anangogwedeza mutu.

Koma Michael anazindikira kuti chinachake chasintha.
Nthawi ya phunziro, Daniel sankamvetsera bwino. Maso ake ankangoyang’ana pa zenera.

Nthawi zina ankadzifunsa kuti mkati mwa kabokosi kaja munali chiyani.

Kodi anali mankhwala osokoneza bongo?

Kodi munali zinthu zakuba?

Kapena china choipa kwambiri?
Mafunso amenewo ankamuvutitsa, koma nthawi yomweyo ankadzikumbutsa kuti banja lake linafunikira ndalama.

Nthawi ya break itafika, Ruth anabwera kudzakhala pafupi naye.

“Wakhala chete lero,” adatero.

“Ndangotopa.”

Ruth anamuyang’ana mosamala.
“Daniel… uli pa vuto lina?”

Daniel anaseka pang’ono koma kusekako kunali kopanda chimwemwe.
“Moyo wanga wonse ndi vuto.”

Ruth anakhala chete kwa kanthawi.
“Usalole mavuto kukusintha.”

Daniel anamuyang’ana mwadzidzidzi.
“Mukamanena zimenezo zimakhala zosavuta chifukwa simukudziwa njala.”

Ruth anadabwa ndi mawu ake.
“Daniel, sindimatanthauza—”

“Khalani chete.”
Ruth anayima pang’onopang’ono n’kuchoka.

Daniel anangotsitsa mutu wake.
Anadziwa kuti walankhula mopweteka.
Koma mkwiyo unkakula mkati mwake tsiku ndi tsiku.

Madzulo atatha sukulu, Daniel sanapite kunyumba.
Miyendo yake inangomutengera yokha ku bus station komwe amakumana ndi Mr. Banda usiku.

Ndipo ndithudi, mwamunayo analipo.
Ankayima pafupi ndi galimoto yakuda uku akucheza ndi amuna ena awiri.

Ataona Daniel, anamwetulira.
“Ndinadziwa kuti ubwera.”

Daniel anayandikira pang’onopang’ono.
“Ndikufuna ntchito ina.”

Mr. Banda anatsegula chitseko cha galimoto.
“Lowa.”

Daniel anazengereza kwa masekondi angapo kenako analowa.
Mkati mwa galimotomo munali fungo la fodya ndi mowa. Amuna awiri aja ankangomuyang’ana chete ngati akumuyesa.

“Uyu ndi mwana uja?” mmodzi anafunsa.

“Inde,” anayankha Mr. Banda. “Amagwira ntchito bwino.”
Daniel anamva mantha pang’ono koma sanasonyeze.

Galimoto inayamba kuyenda.
“Lero ntchito ndi yayikulu,” adatero Mr. Banda. “Ndipo ndalama zake ndi zambiri.”

“Ntchito yanji?”

Mr. Banda anamuyang’ana.
“Kungoperekera chikwama.”

“Kuti?”

“Kwa munthu wina.”
Daniel anangokhala chete.

Mumtima mwake munali mantha, koma njala ndi umphawi zinali kumukokera patsogolo.

Galimoto inayima pafupi ndi nyumba ina yayikulu yomwe inali kumbali ya tauni.
Anapatsidwa chikwama chakuda.

“Usachitsegule,” adatero mwamphamvu.
Daniel anatenga chikwamacho.

Chinali cholemera pang’ono.
“Ngati ndachita bwino?”

“Ulandira ndalama zambiri.”
Daniel anangogwedeza mutu.

Anayenda kupita kunyumba ina yomwe anauzidwa. Panali munthu wovala hoodie wakuda akumudikira.

“watumidwa ndi ndani?” munthuyo anafunsa.

“Mr. Banda.”
Munthuyo anatenga chikwamacho mwachangu n’kupereka ndalama.

Daniel atangotembenuka kuti achoke, chikwamacho chinatseguka pang’ono.
Kwa masekondi ochepa, Daniel anaona zinthu zomwe zinamuziziritsa magazi.
Munali mapaketi ang’onoang’ono a ufa woyera.

Daniel anayima.
Nthawi yomweyo anazindikira choonadi.
Anali kunyamula mankhwala osokoneza bongo.

Mtima wake unayamba kugunda mwamphamvu.

Ankafuna kuthawa nthawi yomweyo.
Koma mawu a Mr. Banda analowa m'maganizo mwake.
"Ulandira ndalama zambiri."

Daniel anabwerera ku galimoto ali chete.
Mr. Banda anamuyang’ana.
“Vuto ndi chiyani?”

Daniel anachedwa kuyankha.
“Palibe.”

Mr. Banda anamwetulira pang’ono ngati munthu amene akudziwa zonse.
“Nthawi zina moyo umatipangitsa kuchita zinthu zimene sitinkafuna.”

Daniel sananene chilichonse.
Atalandira ndalama zake, anayenda kubwerera kunyumba usikuwo ali ndi mtima wolemera kwambiri.

Kunja kunali mdima ndipo mphepo inkawomba mwamphamvu, koma mkati mwa Daniel munali mdima wina waukulu kwambiri.

Atafika kunyumba, Grace anathamangira kwa iye.
“Daniel! Dokotala wabwera lero.”

Daniel anachita mantha.
“Watani?”

“Anati ama ayenera kugula mankhwala msanga.”
Daniel analowa mkati mwachangu.

Amayi ake anali atagona, akuwoneka ofooka kwambiri.
Iye anatulutsa ndalama zina n’kuziika pafupi nawo.

“Tigula mankhwala mawa.”
Amayi ake anamuyang’ana modabwa.
“Ukuchokera nawo kuti ndalama zonsezi?”

Daniel anayang’ana pansi.
“Ndagwira ntchito.”

Amayi ake anangokhala chete.
Kwa nthawi yoyamba, maso awo anasonyeza kukayikira.

“Daniel,” adatero mofooka, “si ntchito zonse zimene zimabweretsa madalitso.”
Daniel sanayankhe.

Mawu awo anamupweteka kwambiri chifukwa ankadziwa kuti akunena zoona.
Usiku umenewo sanagone.
Anangokhala kunja kwa nyumba akuyang’ana nyenyezi.

M’maganizo mwake munkamenyana zinthu ziwiri.

Mbali ina inkamuuza kuti asiye ntchito ya Mr. Banda nthawi yomweyo.

Koma mbali ina inkamukumbutsa kuti amayi ake amafunikira mankhwala, Grace amafunikira chakudya, ndipo iye amafunikira ndalama za sukulu.

Pamene ankakhala chete mumdima, anamva mawu a bambo ake m'maganizo mwake.

"Munthu asalole umphawi umugonjetse."
Koma Daniel anayamba kuona kuti umphawi unali kale utayamba kumugonjetsa.

Ikupitilirabeeeeeeeeeee

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Phalombe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Website

Address

Phalombe