MADEY I

MADEY I

Share

17/06/2025

Unabadwira ku Mwayiwathu Private Hospital, ine ndinabadwira pakhomo kuseli kwa nyumba yathu pa nthochi koma tikukulira limodzi.

Unkaphunzira ku Kaphuka Pvt Primary School,ine ndinkaphunzira pa Chigombe Primary School koma tonse tinakathera ku secondary school.

Unapita ku St Andrew's Pvt Secondary Schoool, ine pa Kabichi CDSS koma tonse tinakathera ku University.

Unapita ku University of South Africa UNISA, ine ku University of Malawi mothandizidwa ndi a mabungwe olipilira ana ovutika koma tonse tili ndi Masters Degree.

Umagona pa bed, ine ndimagona pansi koma tonse timagona pofuna kuthesa tulo.

Umavala zovala zapamwamba, ine ndimavala za kaunjika,.koma tonse timabisa maliseche.

Umadya rosted chicken ndi mpunga, ine ndimadya nsima ya mgayiwa, koma tonse timathesa njala.

Ukuwerenga post imeneyi pa iPhone 13+, ine pa Mobicell, koma tonse timalandira uthenga ofanana.

Note:Lifestyle si mpikisano, anthu tili ndi mapezedwe osiyanasiyana ngakhale kuti tili line imodzi, chisakhale chifukwa kuti a neba anu zikuwathekera mofulumira sizisonyeza kuti inu ndi olephera ayi.

Chimwemwe sichimabwera kamba koti uli ndi china chilichose pa moyowu ayi chimwemwe chimabwera pokhutira ndi zomwe ulinazozo.

Chimwemwe sichimabwera kamba koti uli ndi china chilichose ayi koma posamala ndi kugwiritsa ntchito zomwe ulinazo.

Kumakhutisidwa ndi kangachepe komwe ulinako, osamachita jelous ndi mapezedwe a ena omwe njira zawo simukuziziwa.

06/05/2025

KUYANKHULA KWA NAMADINGO.

Lero ndi tsiku langa loyamba kukhala munyumba yanga muno m'mudzi mwa Wataka, T/A Mlomba kuno ku Machinga. Malo awa ndiwo akhala kunyumba kwanga kuyambira lero mpaka ndidzamalize kumangitsa school block kuno. Ntchito yomanga school block ya utali wa 33x8 meter yokhala ndi ma classroom atatu. Budget ya ndalama zomwe ndilowetse pa project iyi ndi MK 106,059,336.25 (One hundred six million, fifty-nine thousand, three hundred thirty-six Kwacha and twenty-five tambala.

Ndikhala okondwa ndi support ya aliyense pa ine munthawiyi.Mukafuna kukumana nane pamaso bwerani kuno kwa Wataka , T/A Mlomba ,Machinga, Malawi.🇲🇼

Ndatha Ine Wanu,
The White Shirt Village Boy.

Want your practice to be the top-listed Clinic in Machinga?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Telephone

Website

Address

NTAJA
Machinga