Chifundo Trojan Mathado
12/05/2026
ADONA, AKAZI AWO A BWANA ANGA ANASINTHA MAKHALIDWE MOSADZIWIKA BWINO NDIKUYAMBA KUVALA ZAZIFUPI KOMANSO ZOWONEKERA MKATI NDICHOLINGA ANDIKOPE!
KOMA NDIMATI NDINAGANIZIRA NKHANI YA JOSEPH NDI MKAZI WA POTIPHAR BIBLE NDIMAWAPEWA....KOMA MAPETO AKE π
π
£π
π
π
π
‘π
π
π
π
π
π
π
’π
π
π
π
Ώπ
°ππ 4
βοΈ....adonawo anafotokoza motere....
" Monga ukudziwa,pamene titakwatirana ndi wmunangawa,aliyense anabwera ndi mwana kunjira,wawo wamkaziyu ine wamamunayu!
And timakhalako bwinobwino!
Koma pakupita kwa zaka,potengera pressure ya azibale awo komanso amayi awo,abwana akowa anayamba kuvuta,akufuna mwana!
Ine,ndakhala ndikuwauza palibe vuto,poti ogwira ntchitoyo ndiwowo,ndimangodikira pamene azaipote ine mkuima!
Koma ayi,masiku,miyezi zaka mkumachulukirabe opanda mwana wathuwathu awirife!
Mosadziwika bwino,anayamba kusandiyankhula blame,kuti INE nde ndikudziwapo kanthu,ndinatenga kulera mowabisira ndichifukwa iwo akugwira ntchito kma yopanda phindu!
Ndakhala ndikuwayankha kuti INE chibadwireni sinapangepo zimenezo,koma samandikhulupilira kufikira lero timayankhilana zimenezi,mkuyamba kukangana mpaka anandimenya......ineyo ndinakwiya nawayankhula kuti iwo nde Ali ndi vuto...sabereka!
Poyankha anati nanga mwana wangayu?
Ndinawayakha kuti mwina amzanu nde anakuikiranimo kwa akazi Anu akalewo!
Nanga tiziti chiyani,INE ndili bwinobwino and mwezi ulionse ndimaona mwezi bwinobwino....pamenepo Ali ndi bvuto ndi ndani? "
Adonawo anamaliza ndi funso!
Nanenso ndinangoti kukamwa yasa kusowa yankho pa nkhani yawoyo!
Ndinangowapepesa kutonthomza ana mkuwauza akagone,mawa awafotokozere ankhonswe awo za nkhaniyo kuti awathandize!
Nanenso ndinapita kukagona,koma ndili okhumudwa!
Paja njobvu zikamamenyana umazunzika ndi udzu!
M'mawa kunacha,inandidzutsa ndi horn ya galimoto ya bwana,amalowa kumpandako kubwera pakhomo chichokereni usiku uja!
Nditaona,ndi m'mene amaonekera,anali ndi hungover,kusonyeza atatuluka,anapita ku mowa,and aka kanali koyamba kudziwa amamwa komanso kuwaona Ali ndi hungover!
Anangolowa nyumba,kusamba mkutuluka,anandikumbusa zoyenera kuchita mkumapita ku ntchito!
Koma sanabwerenso mpaka m'mawa wa tsiku lotsatilaro!
Madam tsiku limenero sanapite ku ntchito,anali atatupa kumaso,nde sanafune amzawo akawapanikize ndi mafunso,anangopereka report kuti adwala!
Ndinakasiya ana ku school,mkumakapitiliza ntchito Zina!
Zinthu zinasitha pakhomopo!
Abwana,amabwera pakhomo nthawi imene angafunire,pena amatha kugona out 2 days!
Madam ndi ana,amakhala okhumudwa komanso ndi nkhawa moti nane ndinayamba kubalalika kuti izi zikapitilira,sindibwelera kumudzi, chifukwa zinthu zimalongosoka mamuna ndi mkazi akamachita zinthu zogwirizana m'banja!
Awiriwa,ankhoswe atawayankhula,anayamba kugwirizana,koma osati ngati kale,muzambiri samamvana and abwana amatha kumagonabe out masiku ena!
Madam,misadziwika bwino,nawo anasitha zochita,ndimawadziwa kuti ndi mayi ozipasa ulemu!
Akakhala pakhomo,chitenje sichimachoka pathupi pawo!
Koma anasiya,anayamba kumavala zazifupizifupi,oenanso zowonekera mkati abwana akakhala kuti atalikira!
Masiku ambiri,akhala akunditanira ku chipinda chawo,atangovala ngati akukasamba,zonditanira mosadziwika bwinonso ngati izo!
Pena,anagona pa carpet,atangovala kachitenje kowonesa pant mkati....and ndinayamba kudziwa zonsezi akufuna kundikopa,andigwetsere mayesero ine ndichimwe,koma ndimati ndikakumbukira nkhani ya Bible ya Joseph ndi mkamzi wa POTIPHAR ndimawapewa!
Sindimayenera kuchita zimene adonawo amafuna polemekeza bwana angawo!
Ndizotheka,kuwadyera ndalama,atha kundikhululukira,koma kufika powadyera mkazi,imeneyo ikhodza kukhala mudder!
Mkazi,mamuna wina aliyense amamuoanga value kuposa zimene Ali nazo,and sindikanakwanitsa kuchita chinthu chosayeneracho ndi m'mene amandikondera amuna awo!
" Adona,ndi chifukwa chiyani mukumavala mosadzilemekeza masiku ano,kumandionetsa zinthu zimene amuna Anu nde akuyenera aziziona kuchipinda? "
Zitayamba kundinyansa,komanso kutopa ndi kupilira ndinawafunsa adonawo m'mawa wina atandipeza ku kitchen atavalanso mondilawula!
" Ngati ndiwe mamuna,ukuyenera kudziwa kuti ndekuti ndiwe customer wa malonda ndikutsatsawa...komanso ngati chida chako chili cha moyo,ukuyenera kuchigwiritsa tchito..... "
Adonawo anandiyankha m'manso mwawo muli gwaa!
And ine ndinangoti kukamwa yasa,kusowa chonena!
Ndinangosunga ku kitchen kuja mkumakachita zina!
Level inafika pena,adonawo anayamba kumandimasukira kwambiri,kumuyankhula zolawula komanso kufika pomandigwira ndemvu ndi palisani panga ngati akucheza chabe....
Maganizo oipa anayamba kundibwela,koma ndinaziletsabe.
Chiganizo ndinapanga chongowauza amuna awo za khalidweli la aakazi awo lija,koma,ndinali ndi mantha ndi chinthu chimodzi......
π KODI CHINTHU CHIMENECHI CHINGAKHALE CHIYANI?
MULANGIZENI FUNDO ATANI PAMENEPA NANGA ADONA MA PLAN AWO NDI OTANI?
π
£π
π
π
π
π
π
π
£π
π
π
€π
π
!
Β©2026 Chifundo Trojan Mathado The best writer and story teller of all the time!
12/05/2026
π
π
π
π
π
π
π
‘π
π
π
π
π
π
π
π
’?
Tsiku lanu mwaliyamba bwanji?
Jehovah akhalenanu muzochitika zanu zonse! π
Click here to claim your Sponsored Listing.