STAY ALIVE Initiative
27/04/2025
UTHENGA WOCHOKERA KU STAY ALIVE INITIATIVE
Tikhala tikudziwitsani kuti abambo okwana 125 adzipha kuyambira January mpaka March chaka chino. Chiwerengerochi ndichokwera poyerekeza ndi abambo 109 omwe adzipha pa nthawi yomweyi chaka chatha.
Malinga ndi zomwe wachiwiri kwa M'neneri wa Apolisi, a Harry Namwaza, adafotokozera, zinthu monga ngongole, mavuto a mβbanja komanso kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo ndi zomwe zikuchititsa anthu ambiri kudzipha.
Pakadali pano, anthu onse omwe adzipha chaka chino ndi 153 β abambo 125 ndi amayi 28.
Tikupempha abambo onse komanso aliyense amene akukumana ndi mavuto kuti asamadziphimbe ndi nkhawa. Funsani thandizo! Limbikitsani kutuluka poyankhula ndi anzanu kapena kupita kwa maofesi a Apolisi omwe ali pafupi nanu kuti mupeze chithandizo choyenera.
Moyo ndi wofunika β tiyeni tikhale ndi moyo!
Stay Alive Initiative β Kukuthandizani Kukhalabe ndi Moyo.
31/03/2025
Warmest wishes from Stay Alive Initiative! π€ Eid Mubarak to all Muslims around the World! πποΈ May this blessed occasion bring peace, ποΈ joy, π and happiness to you and your loved ones. πβ€οΈ π.
08/02/2025
WAZIPHA NDIPO WASIYA KALATA IYI KU NSANJEππ’
Uyu ndi mnyamata wachichepere kwambiri yemwe wazipha pokumwa mankhwala. Dzina lake ndi Yamikan Junior Thom ochokera kwa Sorgin-Nsanje yemwe amagwira ntchito ngat Agent wa Airtel money ndi mpamba pa stage ya sorgin yopita ku Blantyre. Iye wasiya chibaluwa chomwe chikufotokoza chifukwa chomwe waziphera.
Kwa omwe sitikwanitsa kuona zolembazi alemba kuti" Pepani pepani panalibe kuchitila mwina koma ndinayesetsa ndakanika ngati kungakhale kotheka tidzakumana. Anthu ndili nawo ngongole zawo zambiri,mupange black card yanga ya airtel 0984735183 muli ndalama zambiri pin ndi 2000.
Anzamga nonse ndikusowani ndafera kusaka" uwu nd uthenga wasiya Thom.
Chonde achinyamata kuzipha si solution pezan chithandizo ndi maganizo kwa anzathu osat kuzipha . R I P.
Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.Mzimu wa Jofilisi ukause mumtendere π π
Plz follow STAY ALIVE Initiative
γviralγ·2024fyp
08/02/2025
ππ Tragic Story! ππ
A man took his own life when he discovered the child he raised wasn't his. Now, his wife is left alone, walking around him, and he's no longer there to wonder... "Are there no good women in the world?" π
This story is a sad reminder that life can be tough and unexpected. But we must remember that WE ARE NOT ALONE! π
If you're feeling overwhelmed, lost, or struggling, PLEASE REACH OUT! π€ Talk to someone, share your feelings, and know that there's help available. π
Let's break the silence and support each other. You are NOT alone, and there IS hope! π
Stay Alive, Stay Strong! π
π
08/02/2025
Nkhani yomvetsa Chisoni.π’π
Padakali pano munthu yemwe wazipha pa Manda apa Biwi sakudziwika, ndiye mwina mukhoza kuwazindikira nkhope..
Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.Mzimu wa Jofilisi ukause mumtendere π π
Plz follow STAY ALIVE Initiative
γviralγ·2024fyp
08/02/2025
WAZIPHA KU JONI MDZIKO LA SOUTH AFRICA π
M'nyamata otchedwa Chombe Jofilisi wa mmudzi wa mfumu Mkuziwaduka,TA Mgabu m'boma la Nsanje wamwalira pozikhweza ndi chingwe mdziko la South Africa.
Malinga ndi amene amakhala ndi malemu Jofilisi,akuti iyeyu wazimangilira pa ntchire, dzana masana ku malo otchedwa Stanger mdzikolo, potsatira mavuto omwe amakomana nao komanso kusowa kwa chisamaliro kuchokera kwa abale ake.
Mwa zina malemu Jofilisi akuti wafika ku south Africa ma week atatu apitawa kuchokera ku Mozambique komwe wakhala mmanja mwa a police pafupi fupi miyezi itatu kamba kosowa ziphatso zoyendera ( Passport).
Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.Mzimu wa Jofilisi ukause mumtendere π π
Plz follow @
γviralγ·2024fyp
18/01/2025
Bambo wina wamwalira atadzimangilira m'nkhalango ya bungwe logawa madzi ya Central Region Water Board komwenso kuli Dam m'boma la Kasungu.
Apolisi atafika pa malowa panali kusamvana ndi anthu ogwira ntchito ku bungweri kamba ka ganizo la apolisiwo kuti ayike ntembowo m'nkhalango momwemo ponena kuti lawonongeka kwambiri.
Komabe apolisiwa ngakhale anatero adindo ku bungweri anakana zomwe zinapangitsa apolisi kuchoka pa malopo.
M'modzi mwa anthu omwe anali pa malowa a Isaac Daka anati munthuyo akuwoneka kuti anafa masiku angapo apitawo ponena kuti thupi lake linayamba kuwonongeka komanso limatulutsa fungo.
Pakanali pano anthu ogwira ntchito ku bungweri anyamula thupilo ndipo ati aliyika m'manda a kwa Juma m'boma lomweri la Kasungu.
Osayiwala follow π SSTAY ALIVE Initiative
14/01/2025
WAZIPHA KAMBA KA MAVUTOππ
Yamikani Khifra akwa T/A Nkanda ku Mchinji wazipha kamba ka mavuto omwe akhala akumana nawo.
Khifra wapezeka mnyumba mwake atazimangilira ku Chipinda chomwe amagona.Mzimu wake ukause muntendereπ
Ngati inu kapena wina amene mukumudziwa akufunika thandizo la maganizo, chonde fikirani ku page iyi. Tikhalebe ndi moyo ndi kuthandizana wina ndi mnzake!.
γviralγ·2024fyp
Ophunzira wa pa sukulu ya sekondale ya Chiradzulu CDSS, Shyreen Sowa wa zaka 17 wadzipha pa nkhani zokhudza chikondi.
Ofalitsa nkhani za apolisi mβbomali a Cosmas Kagulo wati malemuyu wachita izi bwenzi lake litamuuza kuti silikumufunanso.
γviralγ·2024fyp
09/01/2025
RIP Georgeπ ποΈ
George wa ku Ekwendeni, Mzuzu, wadzipha atazindikira kuti chibwenzi chake chikumupanga cheat kumbali and amapakulisa kwa munthu winaπ. Ngati mukuvutika, fikirani pulogalamu yathu ya Khala Alibe, muthandizidwa π€. π Simuli nokha π
UTHENGA WOFUNIKA KUCHOKERA KWA HABAKKUK π
Onerani tsopano pamene Habakuku akugawana uthenga wa chiyembekezo ndi chilimbikitso, kutikumbutsa kusankha moyo ndi kupewa zoipa.Ndikukufunirani Chaka Chatsopano chosangalatsa komanso chodala kuchokera ku Stay Alive Initiative! ππ
01/01/2025
Chaka Chabwino Chatsopano! π Chaka chanu chikhale chodzaza ndi chisangalalo & kumwetulira! π Ikani patsogolo thanzi lanu lamalingaliro & thanzi lanu mu 2025 π§ . Tiyeni tilimbane ndi nkhani zamisala limodzi! πͺ
STAYSTAY ALIVE InitiativeToSuicide
Click here to claim your Sponsored Listing.